|
The Apostles' Creed - in Nyanja, Chichewa, Chinyanja |
Ine ndikhulupirira Mulungu Atate wamphamvu-zonse,
Wolenga zakumwamba ndi za pansi pano.Ndikhulupiriranso Yesu Kristu, mwana wake yekha, Ambuye athu,
Amene anapatsidwa ndi Mzimu Woyera,
Nabadwa mwa Maria namwaliyo,
Nazunzidwa kwa Pantiyo Pilato,
Napachikidwa pamtanda,
Namwalira, naikidwa m'manda,
Natsikira ku Gehena.
Mkucha wake Iye anauka kwa akufa.
Anakwera kumwamba,
Nakhala kudzanja lamanja la Mulungu Atate wamphamvu-zonse.
Kuchokera komweko adzabweranso kudzaweruza anthu amoyo ndi akufa.Ndikhulupiriranso Mzimu Woyera,
Mpingo Woyera waChikristu,
Chiyanjano cha okhulupirira onse,
Chikhululukiro cha machimo,
Kuukanso kwa thupi,
Ndi moyo wosatha.
Ameni.
All Languages: http://www.creationism.org/english/ApostlesCreed_Intl.htm
|
|
|
|
|